InfoNow
Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from InfoNow, Digital creator, Lilongwe.
24/04/2026
Mighty Wanderers FC yapeza jersey sponsorship partner watsopano ya ndalama yokwana 200 million kwa chaka kuchokera ku Kingbossi yomwe ndi yogulitsa njinga zamoto. Komano zikuoneka kuti ma "replica" jersey ambiri a consignment ya season ino omwe akugulitsidwa ali dominated ndi 888 bets yomwe zikumveka kuti ubale ndi noma unatha. Practically zikuthauza kuti team idzivala Kingbossi ma sapota 888 bets . Zaka ziwili zapitazo ma sapota amavala ma jersey osiyana ndi omwe ma player amavala yet pogulitsa ankati ndi ma "replica".
Ma "replica" a 888 anabwera ndi inprint yochoka ku factory and anali a season yomwe ino kusonyeza kuti sizinali zodzidzimukila. Kodi kwenikweni panavuta ndi pati kapena zimavuta pati?, Ndiye kuti 888 bets will get free advertising?, Komanso ndiye kuti aliyense obwera amafuna chizindikiro chake chidzikhala kutsogolo kwa jersey komanso large signage? Mosaphweketsa 200 mita, mwina ma team adzilola kit sponsorship ina idzipita ku training kit kapena pa arm.
Paja main sponsor wa league logo yake ikufunikanso pa front pompo ๐
21/04/2026
In search of long lasting peace. They have been here before ๐ฒ๐ผ. Mama Africa---Sad!
21/04/2026
The Golden Era: When MDC United Owned the Pitch. Iyi ndiye imanyapula ma team. Squad ya achina Weston Chifutwe, Clement Kafwafwa, Chiyembekezo Zidana, Grant Lungu, Heston Munthali, Mapopa Msukwa, Thango Chauma, Chrispin Mpesi and others. Inali free scoring team. On this day in 2001 mu Chibuku Cup final MDC inamenya bullets 5-2 mu regulation time.
Tsiku ili Goalkeeper wa MDC Weston Chifutwe anapambadzidwa kunkhope ndi masapota a bullets akuchoka ku dressing room pa half time khani yokhudza "juju" kapena kuti research. Mbali inayi Swadick Sanudi aniyithawa game atachinyidwa zigoli ziwili za msanga mu mphindi zosaposa 12 kuchokera kwa Grant Lungu ndipo analowa Navigator Dzinkambani yemwe naye alandiranso zake zitatu. Pofika mphindi 6 ya mu second half MDC inali itachinya chigoli cha chisanu, eee kunavumba ma botolo sizinaoneke๐
21/04/2026
Rodrick who? Gonani kaye mwatopa ๐
Mighty Wanderers FC edged their arch-rivals FCB Nyasa Big Bullets 1โ0 to lift the season-opening Charity Shield on Saturday at Bingu National Stadium in Lilongwe.
A drop in food prices is relief, but a surge in energy prices is a reminder that the cost of living remains high. ๐ด
07/04/2026
Yemwe adakhalapo mneneli wa chipani cha MCP zaka za m'mbuyomu a Nicholas Dausi adamangidwapo ati chifukwa chopereka uthenga opepesa a Malawi pa zina mwa nkhanza zomwe boma la MCP lanachita mu zaka 31 za ulamiliro oyamba.
Polumikiza nkhaniyi boma linkawazenga mulandu ati ochita upo obisa chilungamo ati chifukwa mwachitsanzo sanabwere poyera kudzaperekela umboni pa mulandu omwe unkazengedwa okhudza kuphedwa kwa nduna komanso phungu omwenso adali a chipani cha MCP ku Mwanza mu 1993.
Panthawiyi iwo anali akugwira ntchito ndi a Gwanda Chakwamba omwe ankatsogolera gulu lina lotsatira MCP ngati President, pamene gulu lina ankatsogolera ndi a John Tembo ngati President.
Panthawiyi boma linawakaniza bail popeza akuti anali asanamalize kufufuza nkhaniyi monga muja zikumakhalira nkhani zambili ngati izi makono.
Ndale za pa Malawi...zina umangoona waziyamba chifukwa ah sizoona๐๐
07/04/2026
Pagolo - Simeon Kapuza
Kumbuyo - James Sangala, Bernald Kalirani, Aaron Nyasulu,
Pakati -Sherry Msuku, Lawrence Majawa, Tendai Mbisa, Gift Zakazaka ndi Mphatso Masha
Kutsogolo - Aggrey Kanyenda ndi Andrew Chikhosi
Apa inakungana size kukana, Double Bees sikanalimba pa Mighty Wanderers FC.
Nowadays, you never really know how matches like these will turn out, especially when playing against less fancied sides.
05/04/2026
Crop iyi atleast โฝ
The Hotel Gate
03/04/2026
Mnyengo ngati yomweyi mu 2002 maule FCB Nyasa Big Bullets anamenya game ndi noma Mighty Wanderers FC mtima uli ku bash yomwe Carlsberg inkachititsa ku Mangochi. Bash inayamba Easter Friday ndipo game inkamenyedwa pa Easter Saturday pa Kamuzu Stadium ku Blantyre.
Game yi inali Charity match ndipo anakonza anali a Women in Business ngati Fundraising. Inali game ya ma temper moti Peter "mjojo" Mponda anapatsidwa Red card. Izi zinapangitsa ma palestina kuopseza referee kuti amukang'antha zomwenso zinapangitsa kuti mpira uyimitsidwe kwa mphindi 30.
Pakutha pa 90 minutes game inathela 1 (Fisher Kondowe) - 1 (Andrew Chikhosi) ndipo bullets sinadikilenso za extra time kapena ma penalty kuti papezeke owina ngakhale zinali zofunika kutero popeza ankaona kuchedwa komanso anangomenyera umodzi omwewo.
Ku bash Captain Jones "speed link" Nkhwazi mothandizana ndi Kumbukani "banya" Lungu anakabandulana ndi ma DJ pandewu yomwe anaiputa Grant "ginte" Lungu atasemphana ndi osakaniza saundiwa.Mwina sankaika saundi yabwino ๐. Tidikila a ginte atiyankhule ๐
.
"Happy Easter" Maule ndi Nyerere.
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Contact the business
Telephone
Website
Address
Lilongwe