MBOBA
Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from MBOBA, Broadcasting & media production company, Dublin.
Mu mbiri ya Malawi apa amapatcha kuti pa mfela nduna
Apolisi ku Mwanza kuno atsimikiza za ngozi yomwe yachitika kwa Liwonde masana a lero pa 29 October, galimoto yomwe amayendetsa Chifundo Minjale (29), CK 5757 Toyota Saloon, yagunda ana 4 pakamodzi, atatu amwalira.
Malingana ndi lipotili, anawa ndi Happiness Tsiliza(8), Tricia Kondwani (7) Blessings Kakowa(4) ndi Hamida Mtepa (7) onsewa a m'mudzi mwa Chikolosa ndipo amaphunzira pa sukulu ya Dalitso PVT.
Lipotili likufotokoza kuti galimotoyi yomwe imachokera mtunda wa Boda kulowera M'boma idaphonya msewu kuchoka ku manzere kupita kumanja komwe idakagunda ana omwe atchulidwa. Atatu mwa iwo amwalirira kuchipatala pamene mmodzi, Blessings, akulandira thandizo la chipatala kutsatira ndikuvulala.
Chifundo Minjale amachokera m'mudzi mwa Benjamin T/A Kanduku konkuno ku Mwanza.
Olemba : Sammey Saulos
Pali mphekesela yokuti ana anayi amene ndiophunzira a pa sukulu ina yolipila ku Mwanza agundidwa ndi galimoto.
Anthu omwe awona ngoziyi ikuchitika afotokoza kuti dalaivala wa galimotoyo amene panthawiyo anali atalawa chakumwa chozunguza ubongo , anaphonya mseu ndikukagunda ana asukuluwo.
Pakanali pano adindo komanso azachitetezo athamangila pa Malo angoziwo.
Tikupatsilani zambiri zokhudza nkhaniyi.
Moses Bingalasi Walota Mwanza Central DPP Shadow MP , anthu amupatsa dzina akuti iyeyo ndi Unstoppable machine.
Olo akangokhosomola anthu akumawombela m'manja, uyu apweteka opikisana nawo uyu Inu.
Ife tidali komko
07/08/2024
Lachisanu lino pa 9 August tidzakupatsilani Zochitika za chipani Cha DPP zomwe zichitike kuchokela mu mzinda wa Blantyre kufikila ku Boma la Mwanza.
Kwakoma ndi kuno
KUMENE KUTI KUKOME NDI KU MPHETE M'MAWA LINO.
Maphunziro komanso zitakataka monga kuphunzila kukonza sopo wochapila ndikusambila mthupi ndi Zina zambiri, zifika pa mponda chimela mawa lino ku mphete m'boma la Mwanza.
Mwa Zina azimayi aphunzila kukonzaso mafuta odzola ,soya pisesi komanso maphikidwe amakono pansi pa chilinganizo chimene akutsogolera ndi Mayi Shadow MP Moses Bingalasi Walota amene ndi a Chipani Cha DPP pansi pa Zokonda Amayi.
Poyankhula ndi Mboba kudzela pa lamya, Mayi Gama a m'mudzi mwa chatha afotokoza kuti pulogalamuyi yawapindulira koposa ndipo mwa Zina akwanitsa kutukula Banja lawo mu ngodya zosiyanasiyana.
Mayi Moses Bingalasi Walota atsimikizanso kuti chilinganizo chotelechi chikhalanso chikufalikila ku madela onse a ku Mwanza kuti miyoyo ya azimayi isinthe ndikupindula ku chochitikachi chifukwa pakadali pano madela oposa khumi ndiwo Ali mu ndondomekoyi , ndipo azimayi onse amene apindula pakadali pano alipo 800.
Wolemba: James Kavala , 07/07/2024 Mwanza
07/06/2024
Mwanza,
Tsopano mwambo wa maliro wayamba ndipo amene akutsogolera ndi a mpingo wa African Abraham komanso amene adyetse mau a Mulungu ndi Arch Bishop M'gona amene ndi mtsogoleri wamkulu wampingowu mu maiko atatu Malawi , Mozambique komanso Zambia.
Mwanza,
Ku Maliro kuno kuli kwayala iyi ndipo ikukondedwa ndi anthu koposa, wotsogolera mwambo akangoitchula kuti ibwere kutsogoro kudzaimba anthu akumachita kuchalira kwinaku makosi m'mwamba kufuna kuwona anyamata ndi asungwana amene akutulutsa mabvume mododometsa khutu la uyo onvela komanso kwinaku akutonthoza ofedwa onse.
By ,Elton G Onart Khanyiwa
07/06/2024
07/06/2024
Mwanza,
Some notable faces in patronage of Mr Bingalasi funeral ceremony here, are of Hon. Nicholas Harry Dausi who is also the member of Parliament of the area, Traditional Authority Kanduku accompanied by village head man Nchotseni.
Reported by , Nashie Tembo
07/06/2024
Mwanza,
Anthu ochuluka akukhamukila ku mwambo wa maliro a Bambo Bingalasi amene akulowa m'manda mu tsiku la lero.
Bambo Bingalasi adamwalira pa 5 sabata yomwe ino atadwala pafupifupi sabata zitatu.
Mwana wawo Moses Bingalasi Walota amenenso ndi Shadow MP wa Chipani cha DPP adatsikimiza za imfayi kudzela pa tsamba lake la Facebook komanso WhatsApp.
Mwambo wa Malirowa ukuchitikila kunyumba yawo ya Malemu Bingalasi ndipo zonse zikatha akayikidwa m'manda mwa Nchotseni .
Reported By: Nashie Tembo
07/06/2024
23/04/2024
Mboba,
MBC kalekale imkatchedwa TVM ndipo kumkakhala ma pulogalamu osangalatsa ochuluka amene sizidali zabwino kuphonyana nawo.
Inde Mafunyeta adali wa ku Mwanza Kuno koma one ndidali ndisadamuonepo kunoko komanso sindimkamudziwa ,mwina chifukwa chokuti iye uja adakulira ku Mwanza West (kwa Chiwembu) asadakhazikike ku Lilongwe, ulendo wanga oyamba kumuwona ndidamuwonela pa kanema ya TVM (MBC now),kenako timkangonva mphekesela yokuti iye uja ndi wathu ndithu, ngati m'mene zimanvekela zokuti Achina Gattah Ase ndiakumwanza kuno zija.
Ife tidadziwa oluso ochuluka kudzela pa program ya Mr sprash inde Geoffrey Kapusa , ndipo ikafika nthawi ya program iyiyi tonse timadzadza m'nyumba kufuna kudyetsa maso ndi mingoli yophukidwa bwino imene Mr Sprash atikonzela
Mr Splash adathandiza oimba ambiliwa kudziwika ku mtundu wa amalawi.
Lero Mr Slash amen ndi Geoffrey Kapusa atisiya m'banda kucha.
Malawi Walira.
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Website
Address
Dublin
Opening Hours
| 9am - 5pm |