Bullets Forever

Bullets Forever

Share

πŸ“’Tsatsani malonda anu ndi Bullets Forever ⚽🚬
Once Maule always Maule β™₯️🀍

24/05/2026

Maule anzanga,, ndi angati mwa inu amene mukufuna kuti katswiri Mike Digital Mkwate waluso ngati Chiomba Nkhanga awonjezere contract yake ndi FCB Nyasa Big Bullets? Ngati mulipo takwezani dzanja tikuoneni.

Mind you kuti ubale wa Mike Digital Mkwate ndi FCB Nyasa Big Bullets wafika kumapeto kwenikweni tsopano koma ma report akuonetsa kuti akukambirana zowonjezera mgwirizano wina watsopano ndi akulu akulu athu.

Osaiwala kupanga follow πŸ‘‰ Bullets Forever page kuti zabwinozi zisakuphonyeni Maule anzanga πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯
❀️🀍⚑πŸ”₯

24/05/2026

Kodi akulu akulu athu amulore Babatunde Adepoju kubwereranso ku FCB Nyasa Big Bullets?

Ngati uli sapota weniweni wa Bullets ukuyenera kupereka maganizo ako pa nkhaniyi.

Ine kumbali yanga ndikuona ngati amulore Babatunde Adepoju abwerenso nanga inu Maule anzanga mukutipo chani pa nkhaniyi?

Osaiwala kupanga follow πŸ‘‰ Bullets Forever page kuti zabwinozi zisakuphonyeni Maule anzanga πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯
❀️🀍⚑

24/05/2026

Good morning Maule πŸ‘‹

Lero mukwera Manoma kapena Ma Banker?

23/05/2026

Defending Midfielder mbambande wasankhidwa kukhala Man Of The Match pa masewero a lero.

Uyu lero watinyamula kwambiri alandire ulemu wake wapadera πŸ”₯πŸ”₯
❀️🀍⚑

23/05/2026

FULL TIME 1-1

Eeeh koma season ino timu yathuyi mmmh zikuvuta kaya vuto nchiyani I don't know 😭

23/05/2026

Maule mwayiona line up yowina? Coach uyu pena amanvatu maganizo anu πŸ˜…πŸ€£

23/05/2026

TIDZIWANE MAULE

Kodi mwakhala mukusapota FCB Nyasa Big Bullets kwa zaka zingati kufikira tsopano?

23/05/2026

Maule anzanga tiyeni tizukute bwinobwino nkhani ya Lungu_the_Baller⚑

Papita masewero angapo chiyambireni season ino osamuona katswiriyu m'bwalo la zamasewero koma amangokhala pa bench nthawi zonse. Season yatha katswiriyu adali a player to watch makamaka akamasewera ngati an attacking Midfielder behind the front line yama strikers.

Now, mukayiona midfield yathu zikuonetsa kuti ndi yobalalika kwambiri chifukwa palibe attack yamphanvu yowoneka ndi maso yomwe ikuyambitsidwa pa central midfield paja nkumapita Kutsogolo kwathu. Nthawi zambili tikumapanga attack yoopsa kudzera m'mbali mwathu momwe muli ma wingers a speed through count attack. Mukaonetsetsa mukhonza kundivomereza kuti adani athu akangotitseka m'ma wing mwathu, timu yathuyi ikumakhala kuti yaferatu.

Kodi kusasewera masewero kwa Wongani Lungu ndi chifukwa choti performance yake silibwino? Kapena mpikisano ndi osewera anzake pakati paja wachuluka kwambiri kotero zikumuvuta kupeza nambala? kapena Coach sakukwanitsa kuyiwerenga game?

Maule tiyeni tikambirane zifukwa zenizeni zomwe zikuchititsa kusapezeka kwa katswiriyu ifetu timankonda Wongani Lungu ndi osewera wabwino yemwe akhoza kusintha zinthu pakati paja.

Osaiwala kupanga follow πŸ‘‰ Bullets Forever page kuti zabwinozi zisakuphonyeni Maule anzanga πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯
❀️🀍⚑

23/05/2026

Blue Eagles πŸ†š FCB Nyasa Big Bullets this afternoon πŸ”₯

Your prediction of the game?

22/05/2026

Malangizo anu ndi otani kwa Coach Gilbert Chirwa pamene tikuyembekezera kukumana ndi anyamata aBlue Eagles kumathero a sabata ino?

Osaiwala kupanga follow πŸ‘‰ Bullets Forever page kuti zabwinozi zisakuphonyeni Maule anzanga πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯
❀️🀍⚑

18/05/2026

Good morning Maule πŸ‘‹
Breaking news ikhale ikubwera shortly khalani pomwepo zachibwana kulibe iyah

Want your public figure to be the top-listed Public Figure in Port Elizabeth?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Website

Address

Port Elizabeth
Port Elizabeth
6000