Onezmo Alka VoiceNation
Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Onezmo Alka VoiceNation, Musician, Zomba.
Agogo anga anandipatsa WATCH ⌚ yampangidwe wachikale kale kuti ndipite nayo malo ogulitsira ma watch cholinga ndikamve kuti ndikhonza kugulitsa ndalama zingati.
Ndinapitadi malo ogulitsira ma WATCH ⌚ nditafika pa malo oyambilira anandiuza kuti WATCH ⌚ yangayi ndimpangidwe wachikale kale mwaicho andipatsa 200. Ndinapitanso pa shop ina kukafunsa ndipo pamenepo anati akhonza kundigula 250 apo Ndinabwelera kwa agogo anga kukawauza mitengo imene ndingagulitsire ..agogo anati fufuzabe mtsika wina usiyanitse.
Ndinapita mmalo ena opanga ma WATCH ⌚ atawona WATCH yangayi anati katunduyi ngwapamwamba koma sitingathe kukugulani mwina mutapita ku MALO kosungira katundu wachikale (museum)
Ndinawuyamba ulendo waku Museum ndipo nditawaonetsa WATCH ⌚ yo anati katundu wanuyi timugula 2 million.
Ndinabwelera kukawauza agogo mtengo waku museum uja. Ndipo agogo anati...NTHAWI ZINA CHINTHU CHINA CHIMAONEKA CHOSAFUNIKIRA MALINGANA NDI MALO AMENE CHIKUPEZEKA....mwachitsanzo 0 ndi opanda ntchito ngati Ali koyambilira kwa nambala 05 ndiye kuti 0 alibe ntchito koma 0 yemweyo kukhala kutsogolo kwa 5 amapanga 50.
Ndinu ofunikira penapake koma mwina chifukwa muli pa malo osayenera mumadzimva kusafunikira ...koma zifufuzeni nokha kuti muli pa malo oyenera kapena mukuzikakamiza kwa anthu omwe sadziwa kufunikira kwanu.
Mulungu sangalenge munthu kukhala osafunikira ayi...ngati ena akukuonani osafunikira vuto si inuyo ayi koma sakudxiwa kufunikira kwanu ndipo kufunikira kwanuko alipo ena angawone siyani kudxidelera nokha
genesis 37v1 ayosephe anali osafunikila pa THAWI imene amakwanisa kumuponya mu ndende kumuponya muchigenje munja
koma atamuzuza THAWI yayitali inafika THAWI imene anakhala ofunika kwambili pa moyo wawo wa azibale ake
ndimafuna ndikutsimikizile kuti adzakufuna amene anakusiyawo mundzina la yesu enanu amuna anu anakusiyani kapena sakukukondani monga mmene munali pachibwezi pano mawabalila ana mwanyasa
enanu azibale anu sakukukondani lelo enanu anthu amakuchepe
Click here to claim your Sponsored Listing.