STORY TIME

STORY TIME

Share

Humble cee the stories writer

Official page

Let's change the world

Follow the page
musicfylite.com for more

Iyi ndi page ya nkhani imene mwini wake ndi HUMBLE CEE page iyi ndiyazilembo zikuluzikulu
Wina akhoza kupanga page yake yofanana ngati yangayi ziwani kuti ndi fake page
Timapanga za nkhani basi palibe zina
Zokhumba zanga ndi kupitisa pasogolo luso la nkhani pangani follow page yanga ndikumawelenga nawo nkhani zathu mosavuta ndi mosangalala

23/06/2026

#πŸ‘Ή *THE WRONG SACRIFICE*β€ΌοΈπŸ‘Ή

Chapter 15

Story Done by

LND CHIKUN✍️Ft STEPHANIE

0998242764/0999739805 *Home of Super stories Gp* INCLUDING *ADMIN PANEL STORY GROUP*
πŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’Ž

_MORE COMMENT MORE SHARE MORE_πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯........

πŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯Ύ

Naye juliana mayeso adali pafupi ndipo chilichonse chokonzekera mayeso a 4 chidatheka , nthawi itayandikira anadabwa osamuona hassan akubwera kudzamupatsa ndalama komanso katundu oyenera ngati zakudya ku boarding , sadadziwe kuti mchimwene wake ali ku m'bindikiro ......

mayeso adayambika , juliana adalemba mayeso mwa chifatse , mtima uli ziiii, ndipo juliana adalibe maganizo achibwana .

tapiwa chifukwa chokondedwa kwambiri ndi apongozi achuma , akakhala kuti wapita kutchuthi amapita kukakhala kwa apongozi olemera kwambiri , komwe amapatsidwa ntchito kumakagwira . apongozi adali ndi ma filling station ndipo amagwira ntchito ngati wa accounts , amakhala ndi mwayi olipilidwa ndi apongozi ake .

nthawi zambiri tapiwa amangoyitanitsira ndalama kwa madalitso posafuna kuti adzimudabwa , cholinga cha tapiwa amkafuna kuti adzamusiye madalitso mwa simple . chiyankhulirane ndi madalitso one week yidatha , adaganiza zoyimba foni yake koma siyimapezeka , .
tapiwa adali ndi account yake yake yomwe nthawi zambiri imakhala yokhuta ndi ndalama . clever
amamupatsa ndalama pa fupi pafupi kudzera ku bank yake nayenso madalitso amatumiza pafupi pafupi ku bank yake .

madalitso samapita pita chifukwa adamunamiza kuti akamabwera bwera adzapangitsa kuti amuchotse sukulu , chomcho madalitso samapitako ayi .

madalitso ma week awiri tsopano adatha , akumidima adaganiza kuti asiye kulimbana naye chifukwa , akapita kunyumba kwa m'busa uja zinthu kukachisi zimaonongeka chimapsa moti adasiya kulimbana naye .

abusa adandiuza kuti , madalitso lero mukaone kunyumba koma musakalimbane ndi zinthu zomwe mudazipeza kudzera muntchito zanu .

m'busa uja adapereka transport kwa , ndidagwira nthumba mwanga ndidangopeza ma pepala wokha wokha shaaaa ndidazifunsa kuti ndalama zilikuti .

adandiveka nikles ya golide yomwe adanditsimikizira kuti ndisamavule olo kosamba .

mumtima mwanga ndidadzimva kupepuka , nthiti zanga zidamasulidwa mchifuwa mwanga mudapepuka .

ndidanyamuka koma foni yanga ndidayisiya komko card yomwe ndimagwiritsa ntchito , adayiwotcha , ndidalibe simcard , moti aliyense samandipeza .

ndidayenda mpaka pa stage pa nthukwa , ndidakwera min bus , ndidadikira kuti idzaze kenako idanyamuka . ndidafika kunamiwawa koma ndidatsika , ndidayenda ulendo wa pagate ndidafika ndidagogoda ngati mlendo , guard adandiyankhuka mwano asadandione .

eeeeee ndati bwana kulibe mubwerenso mawa eshiiiii , . ndidapitilira gogoda , mlonda uja adazikakamiza kubwera pa kawindo kwinaku akuyankhula za mwano , anadula mau atandiona ine nditangoyima .

pepani bwana ndimaona ngati anyamata anu amabwera akuti akufuna malipiro . Gate yidatsekulidwa adapeza kumpanda kutadzadza magalimoto ndi ma bus omwe kusowa podutsa, atafunsa adayankha mlonda kuti magalimoto onsewa ali ndi mavuto , ndi woonongeka . nde antchito onse amakuyimbirani koma phone yanu simapezeka choncho amabwera mudzavuta kuti akufuna malipiro awo .

ndidagwetsa nkhope yanga pamsi , ndidafunsa tapiwa kapena juliana ngati adabwera koma ndidayankhidwa kuti palibe yemwe adabwera koma anzanu aja nde daily akhala akubwera . ndidangodziwa kuti khifra , . m'moyo mwanga sindimafuna nditakumana ndi khifra olo pang'ono.

ndidapeza wantchito ali ku kotazi kwake ndidamuuza kuti andipatsire ma kiyi . atandipatsa ndidalowa mnyumba ndidayenda straight kuchipinda , ndidatsekula draw ya ndalama , ndidapeza kuti mwa dzadza ma tissue matumba anayi , ka mpika kaja mudalibe , ndidatuluka mkumupempha wa ntchito kuti adzandithandize kutulutsa matumba andalama aja , matumba ama tissue onse aja ndidamuuza wa ntchito kuti awa tenge akawa odetse kumbayani .

adayitanitsa wanjinga , adabwera kudzanyamula matumba aja ulendo , . kenako ndidanyamula mafuta omwe ndidapatsidwa ndidapaka paka nyumba yanga komanso katundu yense yemwe adali mnyumba muja . ndidagwada pamsi mkupemphera .
ndili mkati mopemphera ndimadzimva ngati mkono wanga wamanja kwagwada munthu , koma sindidatsekula maso anga . munthu uja ndikamapemphera modzigwedeza nayeso amamveka ngati akudzigwedeza .

tima wanga umalimba kuti ndili ndi mulungu , nditatsekula maso ndidapeza kuti pambali paja palibe munthu aliyense ..

ndidalibe ndalama iliyonse , ndipo agwira ntchito akabwera kuti akufuna ndalama zake , ndimamuuza kuti apeze msika oti ndigulitse galimoto.

chifukwa choti angongole adali wochuluka adayamba kumandivutitsa .
juliana adamaliza mayeso ku sukulu , kuyesera kuyimba foni ya mchimwene wake simapezeka . adakwera nawo galimoto yamakolo anzake yomwe yidamusiya mu tauni . juliana adasenza chikwama chake ulendo wa pa stage . adakwera za kuchilomoni ndipo adatsikira pa filling ya namiwawa , adanyamula kupita kunyumba .

atafika pa Gate mlonda adatsekula mkumulandira , choyambilira adafunsa komwe kuli mchimwene wake , adamulozera mnyumba . adafunsa kuti magalimoto onsewa bwanji , mlonda sadayankhe .

adangodutsa njira zopapatiza kukalowa mnyumba atamunyamulira chikwama .

juliana adalowetsa chikwama mlonda adabwelera pa Gate.
atangolowa juliana , madalitso adamuuza juliana kuti alinaye mawu .

mlongo wanga sukulu wamaliza ndikufuna ndikuuze chilungamo za chuma changa , asadamalize madalitso kuyankhula juliana adayankhula mwa phuma , .
achimwene , agogo adandiyimbira phone akuti chigayo chija chapsa ndi moto wa magetsi moti agogo akukuyimbirani koma foni yanu sikupezeka , komanso ineyo ndimayimba koma foni yanu simapezeka .

ndayesera kuyimbira tapiwa sakundiyankha zomveka , akuti nayenso patenga nthawi osakuyankhulani .

mlongo wanga dekha ndisadayambe kuyankhula tiye tipemphere ......

next part 16..

let's share to all groups

21/06/2026

#πŸ‘Ή *THE WRONG SACRIFICE*β€ΌοΈπŸ‘Ή

Chapter 14

Story Done by

LND CHIKUN✍️Ft STEPHANIE

0998242764/0999739805 *Home of Super stories Gp* INCLUDING *ADMIN PANEL STORY GROUP*
πŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’Ž

_MORE COMMENT MORE SHARE MORE_πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯........

πŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯Ύ
Nditangolowa mkachipinda kaja , prophet adandiyang'ana nkhope yanga ngati mwamantha , sadadziwe chomwe ndimamufunira koma adandiyang'ana mwamantha .

Adandipatsa moni , ndidalandira , kenako adayamba kundifunsa kuti mwabwera ndi mtima onse kapena kudzangoyesa.......

Ndidafunsa kuti ndichani chakupangitsani kuti mundifunse chonchi ,,,,,,,, aaaaaa ndaona ukulu wa satana mumtima mwanu ,. Pepani kuti ndayankhula choncho ,,,,,,, ayi simudalakwitse China ndi choti sindidabwere kudzakuyesani koma ndi mtima onse ,,,,,,,longosola chomwe chakusautsa .

Ndidalongosola chirichonse mpaka kumapeto kuchokera kumaloto mpaka kufika kwa master mkudzafika pomwe ndilipa , . Kumapeto kwake ndidapempha kuti andithandize ndisamwalire ,.
,,ndakumvani nde mwati mpaka adakusinthani dzina kukhala hassan kuchoka ku madalitso ?,,,,,,,, mmmmm pamenepo padalowa ziwanda zazikulu . Komatu mukuoneka kuti ndinu munthu wachuma chochuluka anzanu akumwalira ndi umphawi mungolore kusauka?,,,,,,,,,,, mmmmm atsogo ineyo ndisauke kusiyana ndikuluza moyo ,,,,,,,,, mukudziwa kuti kudziko la midima mukanagwiritsa ntchito dzina la madalitso sizikanatheka??,,,,,,,,oooooh kodi ndichifukwa chake adandisintha dzina eeet?,,,,, eeeeyatu , nde ineyo bambo ngati mwatsimikiza ineyo ndikumasulani koma chimodzi, ndikakumasulani mukhala ndi adani ambiri.

Ndidakhala pheeee , chifukwa nde ndidali ndi anzanga ochuluka kwambiri , koma tsopano anzangawo akakhala adani anga angadzandithandize ndi ndani . Apa nde ndidadekha , chifukwa chakudekha kuja prophet adandifunsa kuti kapena simudakonzeke kukhala ndi adani koma anzanu??

Ndidadziwa kuti ndikakana , anditenga ngati ndidadzamuyesa , ndidamuuza kuti , ndikuvomera kuti anzangawo asanduke adani.

Adapitiliza kuyankhula ok, ndiye tigwade pamsi tipemphere chifukwa apa tikulimbana ndinkhondo yoposa msinkhu wathu choncho tiyitane mzimu oyera komanso kuchotsa malire omwe adayika mwaiwe okhudza imfa .

Tonse tidagwada , ndidayamba kudzimva kulemera mchifuwa mwanga , abusa adangofikira pa kolasi pa marilime. Adapemphera atangoyamenya timapemphero kudziko lachilendo kudadzidzimuka , . Master idayamba kumva kutentha kumapazi , timatambula ta galasi timasweka mkumagwetsa magazi , kudavuta kukachisi , fungo la anthu omwe adawapha lidayamba kumveka paliponse ngati tear gas β›½.

Mwachangu master adatenga chimsalu kuti awone chomwe chimapangitsa , adaona maso a madalitso akutuluka misonzi koma ali chitsekere , pambalipa pali m'busa odzodzedwa kuswa pemphero .

Nthawi yomweyo chimsalu chomwe amaonerapo zinthu chija chidayamba kutuluka utsi , master adadziwa kuti hassan wa atembenukira .

S**t adayitanitsa mkumano wa akulu akulu okha okha , mwachangu adafika , . Nde zomwe zimachitika amatumiza m'modzi m'modzi pa malo omwe amapemphera hassan kuti akatumize mphezi . Munthu oyamba adayima kutsogolo kwa abusa ndi hassan , kenako adaponya mphezi yomwe yidawagwedeza abusa kukhalanga akufuna kugwa koma manja onse ali m'mwamba atagwira bible , sadasiye kupemphera molumikiza , mu bible mudatuluka moto omwe udanyeketsa munthu uja mkusowa , . Mene amafika kumidima mkuti alibe chovala atatsala ndi bombasa eshiii moto wamzimu oyera utamuwotcha. Koma akuoneka mwamantha akungonjenjemera adafika pa kagulu komwe kadali ndi master .

Wina adathamanga ndi chimsalu ndikumukuta . Azibambo omwe adali ndi master aja onse adapsa mtima ndi zomwe zidamuchitikira nzawo .

Winanso adasowa kukapezeka mkanyumba komwe kadali abusa ndi hassan , nkhondo yolimbana ndi hassan yidayambika kudziko lamizimu . Nthawi yomweyo ka mphika komwe kadali kunyumba kwa hassan kadasowa , ndalama zomwe zidasungidwa m'matumba zidasanduka ma tissue .

Kudali nkhondo , kupemphera molimbika , munthu uja atafika mkachipinda kaja , adayamba kuziponda ponda ngati akupsa ndi moto , chifukwa chakumva kupweteka palibe chomwe adapanga koma kungosowa , . Kanyumba kaja konse anayaka moto koma m'busa ndi hassan moto uja samaumva kapena kuona . Aliyense wa ntchito zakumidima amaona moto basi , . Master adalamula kuti onse apite ma kwawo kaye , apitiliza mawa , amayankhula izi poganizira kuti , hassan aphweka akapita kwawo .

Abusa aja amachita kutuluka thukuta ndikupemphera , milomo yawo m'mbali mwake mumatuluka phala loyera .

Hassan nthiti zake zimapweteka ngati wagwidwa ndi chibayo , mchifuwa mwake mumalemera . Abusa adayamba kutsitsa mawu koma akumveka ngati asasa , kumapeto kwake adayankha kuti amen.

Abusa adandifunsa kuti ndikumva bwanji ?, abusa ndikumva ngati chibayo mchifuwa mwanga mukulemera , pakhosi pakumveka ngati pa dzadza makhololo , koma ndikatsokomola sakumveka ngati makhololo , . Abusa adandiyang'ana. Kenako adayankhula kuti uli ndi week uli kuno , uli munkhondo yayikulu , akukusaka kwambiri , ndaona kuti udabwera pa galimoto ukatuluka panjapo uyang'ane pomwe udayimika galimoto yako .

Ndidakhala pheeee kulingalira , ndidangodziwa kuti nkhondo yolimbana ndi umphawi ndauyamba .

Abusa adatulutsa mafuta omwe adandipaka pa chipumi .
Adandiwonetsa malo ogona mnyumba mwawo , chipinda ichi muzigona umu koma musadagone mudziwaza madzi awa ali mkabotolowa .
Nditatuluka panja ndidaona galimoto yanga palibepo eshiiiiii , ndidachita kudziwiratu kuti kwa master akundipanganira .

Mtima wanga umapitilira kugunda kuganizira kuti kunyumba kwanga kulibwanji ?.

Kusukulu tapiwa adayiwara kuti kuli madalitso , adakomedwa ndichikondi kwa clever , tapiwa adapita ndi clever kukaonekera , koma kwawo adanama kuti hassan ndi iyeyu banja lidatha adavomereza ndipo clever amapititsa chithandizo ngakhale tapiwa asakudziwa . Pena amapita kwa clever tapiwa kukakhala week ngati kwa apongozi ake , .

Naye juliana mayeso adali pafupi ndipo chilichonse chokonzekera mayeso a 4 chidatheka , nthawi itayandikira anadabwa osamuona hassan akubwera kudzamupatsa ndalama komanso katundu oyenera ngati zakudya ku boarding , sadadziwe kuti mchimwene wake ali ku m'bindikiro ......

Next part 15.....

Let's share to all groups

17/06/2026

#πŸ‘Ή *THE WRONG SACRIFICE*β€ΌοΈπŸ‘Ή

Chapter 13

Story Done by

LND CHIKUN✍️Ft STEPHANIE

0998242764/0999739805 *Home of Super stories Gp* INCLUDING *ADMIN PANEL STORY GROUP*
πŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’Ž

_MORE COMMENT MORE SHARE MORE_πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯........

πŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯Ύ

Mfumu idatutumuka kuyamba kufunsa dzina lake kwa nzake yemwe adabwera naye kudzayamba kupembedza . Why hassan sakupezeka ,,,,,,,,,, ndekuti wangotanganidwa,,,,,,,,,ayi ...ayi ndikumuona kuti sali otanganidwa , adatenga chimsalu chofiira mkumuyang'anitsa anthu aja adamuona hassan wangokhala pa mpando .

Kenako mfumu adayankhula mau achizungu kuti see mkono akutambasulira kuchimsaluko .....

Anthu onse adali odabwa moti adayamba kumuganizira , panthawi yomwe madalitso adangokhala adali akudya mutu kuganiza kuti apange bwanji kuti asamwalire , . Nayo mfumu yakumadzi yidatuma nzake yemwe adapita naye tsiku loyamba kuti akamufufuze kuti chikuvuta ndi chani. Khifra sadamvetse adazifunsa mafunso , koma hassan akuganiza bwanji , munthu umalemekeza pomwe ukudyera , nanga mpaka kulephera kupita kopembedza mfumu waganiza bwanji, munthu adali olimbikira.

Khifra adanyamuka , sadafune kuti akambirane naye pa foni , atafika adatsekula Gate mlonda popeza galimoto ya khifra amayidziwa .

Khifra adalowa kukapanga Park pomwe pamayima hassan ndigalimoto yake , mlonda atatseka Gate adathamangira pomwe padayima galimoto ya khifra .

Mwaswera bwanji?,,,,,,, taswera bho bro , koma hassan alipo?????,,,,, aaaa nde mwangosemphana pompano akutuluka kumene ,,,,,,,aaaahh nde ndimuyimbire foni waiting.

Kuruu..kuruuu. yes khifra hello ,,,,,,,,, yes broh ulikutiko??,,,,,,, aaaaa ndikupita ndikamuone sister ku sukulu ,,,,,,,aaaa ine nde ndafikatu pa home kwanu ,,,,,,,,,ooooh ok basi ndikubwelera .

Hassan asadaganize zochokapo amalingalira kuti agwiritse ntchito njira yiti kuti asamwalire , . Oooooh s**t ndidamva za abusa ena ake ku chilomoni , adadzutsapo wakufa ndipite komweko . Adatuluka panja kukatenga galimoto imodzi mwama galimoto ake ochuluka omwe adali pa khomopo . Adateluka Gate, mkuyamba ulendo .

Master sadanene kuti imfa ya hassan idzakhala yotani izo sadaneneletu .

Ulendo uli mkati foni idayitana , ndisadayankhe ndidapanga check kaye mkono umodzi uli pachiongolero , khifra ooooh , maganizo adandipeza kuti foni ya khifra mkutheka wamuona kuti akupita kwa abusa mchifukwa akuyimba . Ndidadziyankhulira kuti eshiiii koma chuma ichi chitiwonetsa zinthu.

Ndidayika kukhutu ndipomwe timayankhulana ndi khifra, koma ndidamunamiza kuti ndikupita ku sukulu kwa mlongo wanga , komabe adazikakamiza kuti atha kunditsatira , koma sadakambe chomwe amandifunira .

Ndidakhotetsa galimoto mwachangu kutenga msewu wa Blantyre koma ndikuthamanga , apa mkuti phone yanga ili ku khutu kumuchedwetsa khifra ndi tinkhani , cholinga ndithe mtunda ndikapezeke pa HHI . Ndidafika pa clock tower ndidamuyankha kuti atha kunditsatira koma achite mwachangu , kenako ndidadula foni .

Ndidayendetsa galimoto mpaka ndidafika pa HHI pafupi ndi round about .

Ndidayima pa HHI stage kudikira khifra , koma pena nkhawa imandipeza kuti why khifra akundifuna , I think mkutheka wadziwa zomwe ndikuyendera.

Sindidadziwe kuti nthawi yomwe ndimaona ngati ndikumuchedwetsa ndi nkhani pa foni sindidadziwe kuti khifra adali atayamba kale kuyendetsa galimoto moti sindidakhale kwambiri pa HHI paja , ndidango dabwira galimoto ya khifra ikudzandi imira ku tsogolo , . Mtima udagunda . Nthawi yomweyo ndidatsika mugalimoto yanga kupita kukamuyimilira pachitseko cha galimoto yake , adandilozera mbali ina ya chitseko chake kuti ndikwere tikambirane , ndidapita kuseri komwe ndidakatsekula mbali ya chitseko ija mkukwera .

Ndidamwetulira mozikakamiza kwinaku ndikuyankhula zokhudza iye kuti wasowa .

Eshiii khifra mudanditayatu kusowa kumeneku ,,,,,,,,, anthu okwatira inu kumafunika kumakupatsani nthawi yoti mudzicheza ndi azikazi anu kkkkk,,,,,,,,,,,kkkkkk khifra eshiiiii mavuto ndipo ndikadadziwa sibwenzi nditapanga ,,,,,,,,,bwanjinso ,,,,,,,, nthawi zambiri mkaxi uja amandipatsa ma stress eshuuuu,,,,,,,,,, oooooh mchifukwa chake wasiya kubwera kudzapembedza mfumu eeet ,,,,,,,,,aaayinso kungoti....,,,,,, waiting hassan tikambirana nkhani imeneyi pano mpanjira tiye tikamuone kaye mlongo wakoyo then tidzibwelera ,,,,,,,,,,, ok chabwino .

Ndidatsika galimoto ya khifra kukalowa mugalimoto mwanga , mtima wanga udadzimva kuti uli omangidwa zikuoneka kuti khifra wabwera ndi milandu yovuta kuyankha.

Ndidakatsekula galimoto yanga mkudzitsekera , kenako ndidayamba ndine kunyamuka pa stage, khifra mkumabwera pa mbuyo panga . Tidazungulira pa round about kenako tidatenga msewu waku BSS khifra amangondilondora, ngakhale ndimapita kusukulu kwa julian ndidalibeko nako ma plan chifukwa ndikana khala kuti ndinali nako ma plan bwenzi nditamugulira zinthu , koma ndidangokhaniza zokamupatsa ndalama .

Tidafika pa Gate mlonda adatsekula , tidayenda mpaka tidakapanga Park pa bwalo la office , ndisadatsike ndidaona aboarding master akubwera pa fupi ndi galimoto langa , hello sir , ndidadabwa anthu akundilozerana , amvekere mwini wake wa ma bus a hassan uja ndi uyo .. eeeya koma nde ndiwachinyamatatu ,, eshiiiiii koma ali ndi doller eshiiiii ndalama zopereka mseru ,, kodi sukudziwa kuti mlongo wake tili naye pompano?,,,,,, mmmmm mkutheka ndiwosiyana mayi nanga mlongo wake weni weni angamaphunzire ya boma inu ,,,, eeeti eeti ndili ine ndikanamupititsa ku bakhita kubalaka iiiya azidya m'gayiwa kuno!!?? ,,,,,, mmmm guys nthawi zina limakhala dala kuti akule munzeru.

Kufika kwanga koma mwini wakene sindimadziwa , ndimangodabwa ana asukulu atsikana ndi anyamata kumandiloza loza ena kumandisuzumira m'makalasi .

A boarding master adayitana mwana wa sukulu wina kuti amuyitana Julian, apa ndidayamba kucheza ndi aboarding master ndi khifra , ndimafunsa za status ya juliana ku sukulu , koma amanditsimikizira ndithu kuti ndisamukayikire mlongo wanga , tili mkati mocheza. Kudatulukira juliana a boarding master adatsanzika kwinaku akuyankhula nkhani zomsele wula juliana ngati mchokero , mene amachoka tonse tidatsala ndi phwete .

Ndidatsala ndi Julian naye khifra sadachoke , eehe ndalama izi mugwiritse ntchito weekend musabwere kunyumba pajatu kunyumba kudakuyandikira ,,,,,,,kkkkk aaa nanga ndidzikhala ngati kwathu mkutali , ,,,,,,, ukufunika ndikupezere sukulu yakutali iwe . Onse adaseka , naye khifra adatulutsa ka mfwafwa kake kopinda kamodzi mkumupatsa juliana , tidamulimbikitsa za sukulu kenako tidanyamuka pa malopa . Macheza omwe tidacheza kusukulu kuja , mtima wanga udakhala pamsi kuyiwara za milandu yomwe khifra adabweretsa ngakhale asadandiuze . Tonse tidakwera mumagalimoto athu ulendo wakunamiwawa , nditafika pagate ndi dalowa nayenso khifra adaliwa kukapanga Park pafupi ndipomwe ndidapanga Park.

Tonse tidatsika nkhani zili pakamwa kukalowa mnyumba .
Tidakhala pa mpando wantchito adathamanga ndi madzi komanso tizakumwa .

Nkhani idayamba kuchokera kwa khifra . Hassan masiku ano sukumapita ku temple bwanji?,,,,,,,, eshiiiii kutanganidwa broh ,,,,,,,,, ngati master adakufunsa pa menepo sipali bwinotu. ,,,,,,, simukunama ,koma khifra zimenezi ungazituluke bwanji?,,,,,, what?,ulindimaganizo otuluka chonsecho udalonjeza?,,,,,,,,,,ayi ndimangofuna kudziwa,,,,,,,,, pa chimenechi master sizingamukomere atha kukupanga chipongwe,,,,,,ndati ayi khifra sindingapange ,,,,,,,, koma sukumabwera bwanji,,,,,,,this week ndifika patengadi nthawi ndisaname ,. Ngakhale ndimayankha koma mtima ukukana , tidadya chakudya tidacheza , nthawi yokayendera ma business athu idafika , tidatsanzikana , ine m'malo mopita mtauni kukayendera ma business ndidatenga msewu wakuchilomoni kukakumana ndi prophet , ndidayimba foni ku ma office anga onse ama business kuti sundibwera , apa mkuti ndalama zanga zonse zambiri zili ku ma Bank,

Ndidasiya ku bank chifukwa ndimaganiza kuti akadzandilanda ka mphika kaja , akukachisi ndidzatsale ndi ndalama zaku ma Bank.

Koma mtsuko uja umatulutsabe ndalama zodzadza ndindalama .

Ndidayendetsa galimoto foni ili kukhutu kufunsira map kuchokera kwa mwini wake prophet.

Mwazisomo ndidafika . Ndidalowetsa galimoto kumpanda kwake , kudabwera anyamata ake a prophet kudzandi tenga kupita nane kuka office komwe kudali prophet.

Nditangolowa mkachipinda kaja , prophet adandiyang'ana nkhope yanga ngati mwamantha , sadadziwe chomwe ndimamufunira koma adandiyang'ana mwamantha .

Adandipatsa moni , ndidalandira , kenako adayamba kundifunsa kuti mwabwera ndi mtima onse kapena kudzangoyesa.......

Next part 14

Let's share to all groups

09/06/2026

#πŸ‘Ή *THE WRONG SACRIFICE*β€ΌοΈπŸ‘Ή

Chapter 12

Story Done by

LND CHIKUN✍️Ft STEPHANIE

0998242764/0999739805 *Home of Super stories Gp* INCLUDING *ADMIN PANEL STORY GROUP*
πŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’Ž

_MORE COMMENT MORE SHARE MORE_πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯........

πŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯Ύ
Hassan tsiku ndi mwezi wakufa adauzidwa ndi mfumu yakumadzi , mantha adayamba kumugwira hassan .......

Amamugwira akaona kuti zikuyandikirandithu .
Hassan chuma chudamuyanja thupi lidasintha kwambiri , omuyandikira amadyelera , hassan tsopano adali ndi abwenzi ambiri.

Mnyumba mwake mudali wa ntchito wamamuna yemwe adali dolo kumbali yazophika phika , wagwira ntchito ma hotel akulu akulu muli longwe komanso ku Blantyre, wantchito wina adali special wokhonza mnyumba. Adaonjezera azilondo ena olondera galimoto kuti adzisinthana , hassan ndalama sizimatha ayi zimangokumana matumba matumba , koma ngati uli mdalitso nzathu adaupeza kwambiri , ku bank ma account mudali ndalama zochuluka kwambiri.

Juliana amalimbikira maphunziro poganizira umasiye wake , naye tapiwa amalimbikira ma phunziro ake ku CU . Tapiwa pa collage adali mkazi wa ma looks a sharp , thako lidali mmenemo , aliyense amaukha dovu kufunitsitss kumufunsira .

Tapiwa amalandira ma calls achilendo mufoni mwake daily anyamata kufuna kuyesa mwayi .

Kufuna kupanga chibwenzi umangokhala mtima koma kunena zoona tapiwa samasowa kanthu , hassan amayesetsa poganizira umphawi wakwawo kwa tapiwa . Azibale ake atapiwa alongo ake omwe adasiyira sukulu pa njira onse adawabwezeretsa kusukulu .

Naye juliana ngakhale adali ku sukulu yotchipa koma amanjoya , every weekend hassan amabwera kudzamupatsa ndalama komanso kutundu wina oyenera ku sukulu pa moyo wa mwana wa boarding.

Mayeso aphunzitsi adalemba julliana, adakhonzera form 4 chaka .

Hassan ichi chidali chaka chomaliza kukhala ndi chuma komanso kukhala ndi moyo .

Atapita kwa mfumu adamuuza moyenera , November pa 26 ndi chaka chomwe udzaluze moyo .

Nthawi yomwe amakhala amadziwa ndithu kuti ali pa ulendo . Koma malingana ndi ulemu omwe amalandira akamayenda munzinda wa tauni , chifukwa adafika pomayenda ndi ma body guard paliponse, . Choncho amazimva kuti sakuyenera kumwalira moyo ukukoma .

Naye tapiwa adalowa level 2 yamaphunziro ake , tapiwa pali mamuna wina yemwe adali woneka bwino komanso amachokera kubanja lodziwika ndi makobidi , adagwa naye mchikondi adayesetsa kukana amuna ambiri koma pokhapo sadapitilire , iyeyo amasilira pairing yaku prep imamuwaza komanso ena akamanyada kuti wagwiritsa bere iye amasilira kwambiri,. Amatha miyezi ingapo asadaonane ndi hassan , choncho amafuna wapafupi kuti azizithandizira pafupi .

Mwachidule adamulora clever , chibwenzi chimayenda ndithu nthawi zambiri amakakumanirana kuma hotel wodula kwambiri , amayendetsedwa pa galimoto ndi clever akamapita ku hotel aliyense amadziwa za chibwenzi chimenechi . Amagayirana ma million . Tapiwa amamupatsa ma million bwenzilake naye clever amapereka ma million kwa tapiwa.

Pa ng'ono pa ng'ono adayamba kuyiwara chikondi cha hassan , kuyimba foni kwa hassan ngati kale kuti ndakusowa ndachisowa chikondi chako zonsezo adasiya ndithu , adali busy ndi clever mpaka adakamuonetsa kwawo .
Naye clever adamutengera tapiwa kwa makolo ake , moyo udali wokoma . Nthawi zina hassan akapita kukamuona , amamunamiza kuti driver wakwawo hassan not mamuna wake.

Akapita kunyumba tapiwa adasintha amamuyankhula zichewa zakusukulu kwawo zomunyoza koma hassan osamazindikira . Mumtima mwa tapiwa amati akufuna kudzakwatiwa ophunzira okha okha .

Pena julliana zimamu bhowa zomamunyozera mchimwene wake iye akumva .

Naye hassan adayamba kumudabwa nkhalidwe lake la tapiwa lomwe amapanga. Hassan lidayamba kumunyansa chifukwa ngakhale antchito tapiwa samawayankhula bwino.

Izi zimachitika atabwera onse ku holiday yoyamba mchaka chomwe hassan adali nacho ndi chiyembekezo yayifa ,eshiiii tapiwa adagena .

Hassan amakhala mwamantha ndi imfa yake , mchifukwa chake mulungu adatibisira tsiku la imfa amadziwa kuti tikhonzekera kuyizemba munjira zosiyana siyana , choncho hassan adayamba kumumvera chisoni julliana, kuti akhoza osamaliza sukulu chifukwa cha imfa yake , pamene tapiwa zake zayera olo atamusiyira pomwepo akhonza kukasaka ntchito mkumakathandizira azibale ake .

Aaayi sindingamwalire mophweka no..no..no. tsono vuto lidali loti akangomwalira chuma chija chisokonekera pakamodzi adayamba kudya ma plan .

Ganizo loti are adayamba kulisintha , bwanji ndisauke ndili moyo kuti ndizigwira ma ganyu ndipitilize kumulipilira mlongo wanga .

Chifukwa chakukana kufa adayamba ku jomba kokapembedza mfumu ija . Masiku angapo , mfumu ija idatutumuka , chifukwa amamuyang'ana momutsata kwambiri chifukwa choti chaka chimenecho amafunika are ndithu .

Mfumu idatutumuka kuyamba kufunsa dzina lake kwa nzake yemwe adabwera naye kudzayamba kupembedza . Why hassan sakupezeka ,,,,,,,,,, ndekuti wangotanganidwa,,,,,,,,,ayi ...ayi ndikumuona kuti sali otanganidwa , adatenga chimsalu chofiira mkumuyang'anitsa anthu aja adamuona hassan wangokhala pa mpando .

Kenako mfumu adayankhula mau achizungu kuti see mkono akutambasulira kuchimsaluko .....

Next part 13....

Let's share to all groups

04/06/2026

#πŸ‘Ή *THE WRONG SACRIFICE*β€ΌοΈπŸ‘Ή

Chapter 11

Story Done by

LND CHIKUN✍️Ft STEPHANIE

0998242764/0999739805 *Home of Super stories Gp* INCLUDING *ADMIN PANEL STORY GROUP*
πŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’ŽπŸ’Ž

_MORE COMMENT MORE SHARE MORE_πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯πŸ”₯........

πŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯ΎπŸ₯Ύ

Kenako adatembenukira ku boot kuti amupange welcome mlamu wake , ndidangoona tapiwa wayima akungomuyang'ana juliana naye juliana adayika chikwama pamsi mkudzayima kumuyang'ana tapiwa . Mafunso adakumano .
Tapiwa?,,,,,,juliana?....

Juliana samamvetsa kupezeka kwa tapiwa kunyumba kwanga ,. Juliana ndi tapiwa adakumbatirana , kenako tapiwa adanyamula chikwama cha juliana akusangalala , adakwera ma steps mpaka mnyumba .

Ine ndidali ndikusamala mugalimoto muja kuti ndichokepo ndidali ndi ulendo opita kwa mfumu kukapembedza .

Macheza adaphulika . Juliana sadadziwe kuti madalitso adasintha dzina ndi hassan. Mmmmm atsikana mulipo?????,,,,,,,, ineyo ndilipo kwambiri moti tidangobisala kumudzi,,,,,,,,, koma iwe tsono uyu ndindani wako mesa ulindi mlongo wako m'modzi madalitso?,,,,,,,,, eya kkkkkk tilipo awiri ,,,,, nde madalitso alikuti ???,,,,,,,,,,tsono ukukhala nayeyu ndindani ?,,,,,,,,,mmmmm uyutu ndi hassan,,,,,,,, mkutheka adachita kusintha dzinalo ,,,,,,,,, you mean kuti uyu ndi madalitso??????,,,,,,,,,eya komanso zoti mlongo wanga adakwatira kwathu sadawafotokozere agogo iweyo bwanji?,,,,,,,,, mmmmm program ilipo yobwera kwanu ,,,,,,,,,, eshiiii tapiwa wakwatiwa mmene ulilimu ndiwe nzanga wachichepere sukulu bwanji?,,,,,,,,, long story koma mwachidule ndingoti ndidabwera pano ngati wantchito , ndimasaka ndalama yoti ndipitire kusukulu , makolo anga onse nane adabwalira ndiye tidapita kumudzi ,,,,,,,,,,,, iwe aphunzitsi anga a part time adamwalira?,,,,,,,,,,,kkkkkk koma ndiye umakumbukiratu kkkkkkkk,,,,,,,, iwe sindimayiwala ine eshiiiii ubale wakwanu ndi wakwathu udali olimba , imeneyi idzakhala history kutsogoloku .

Anthuwa amakambirana atakhala pa sitting room, madalitso sadavutike mkulowa mnyumba adatembenukira panja pompaja kupita kwa mfumu kukalambira poti m'dima udali utayamba, atsikanawa samadziwa komwe madalitso adapita chifukwa maganizo awo adali woti mada ali panja .

Hassan kwa mfumu adamuuza kuti atsikana omwe alikunyumba kwake akufunika asamalitse nawo .

Tapiwa adatuluka panja kukayang'ana madalitso koma sadapezepo galimoto adafunsa mlonda adayankha kuti atuluka panja . Kenako tapiwa adalowa mnyumba , adamuonetsa juliana chipinda chogona chake , kenako adapita kukapanga zakukhitcheni onse kwinaku akukumbutsana , za anzawo omwe amkasewera nawo akukhala kuchilimba .
Monga anthu osowana kumakhala kukamba nkhani ndithu za kale kale.

Madalitso adatulukira, pena pake tapiwa amakhala ndimafunso maka pakayendedwe kake ka madalitso , timaulendo yititi samatsanzika , komanso sadalongosolepo kuti ntchito amagwira kutiko komanso chuma chake adachipeza bwanji .

Mfumu ija po muwuza kuti asamale ndi atsikana alikunyumba kwake yidali yitawunguza kale .
Atafika madalitso . mumtima mwa tapiwa mudadzadza msanje yayikulu , koma sadafune kudzionetsera . Amakonza chakudya kuchiyika pa tebulo . Madalitso atawona kuti atsikana atanganidwa mkucheza kwinaku akugwira ntchito , adaona kuti ndinthawi yoti akatolere ndalama kuchipinda, adangoditsa pa sitting room kupita ku chipinda kukatsekula mu drawer kulongedza ndalama nthumba .

Atangomaliza kulongedza ndalama zija kuti adzitseka chitseko chakuchipinda chidatsekulidwa , apa mkuti madalitso atangomaliza kumene kutseka drawer koma adali asadasunthe makiyi a drawer ali m'manja.

Tapiwa adangoyima pakhomo kumangomuyang'ana mwachidwi madalitso naye madalitso amamuyang'ana tapiwa mwachidwi.

Mtima wa madalitso udayamba kumuwawa , adakumbukira mau a mfumu ija , amadzimva kuti tapiwa wayamba kumulonda Linda any time amusokonezera chuma .

Tapiwa adafunsa mwamsanje , mwayamba zibwenzi ?,,,,,,,,,, what is it?,,,,,,,,,komanso mukuoneka anthumanzi bwanji ?,,,,,,,, waona udyo ,,,,,,,,,tsono pomwe mwayimapo mesa ndi drawer ya Eni wake ?,,,,,,,,, iwe dekha ndangoyima pano ,,,,,,,,, ok tiyeni mukadye ,,,,,,, koma wayiyambayo ndiyokhota osamandilonda Londa ngati pochoka ndimanyamula nyumba ine .

Tapiwa adamuyang'ana madalitso kenako adatuluka mkutseka chitseko chakuchipinda kumusiya madalitso atangoyima .

Madalitso adapumira m'mwamba kwinaku akudziponya pa bedi kuganiza zoti achite .

Adaliza zala za m'manja ngati akuswa mtedza . Thwaaaa tapiwa akufunika boarding , mapeto ake andisokonezera zinthu zanga uyu .

Kunena zoona tapiwa adali wanzeru kwambiri , masiku awiri anadutsa , tapiwa ndi julliana akukondana . Panthawiyi mkuti juliana asadayambe sukulu pamene tapiwa amapita kusukulu motengedwa ndi driver wake mamawa uliwonse pankhomo pamatsala juliana yekha . Masiku wotsatira madalitso adamutengera mtauni juliana kukamugulira katundu wochuluka wakusukulu kuphatikiza kukamusokotsera uniform.

Adamuyika mugalimoto mkumabwelera , tsiku lotsatira adatenga transfer latter kupita nayo ku BSS , uko sizidavute , adamutengera kuma hostel.

Kenako tapiwa adamusakira sukulu ya private koma ya boarding, onse adapita ku boarding, pakhomo padatsala madalitso ekha , . Madalitso amamukonda tapiwa naye juliana amamukonda mlongo wake . Madalitso adamanga chigayo kumudzi ndipo chidayamba kugwira ntchito ,
Adagula magalimoto omwe amapangitsa ma hire ma company ngati car hire , adamangitsa ma shop munzinda wa Blantyre omwe amapangitsa rent , adamangitsa chipatala chomwe chimagwira ntchito ngati cha private .

Masiku nde amapita adalowa chaka cha chitatu adatsala ndi zaka ziwiri , juliana ndi tapiwa amasuntha ma kalasi .
Tapiwa adakalowa form 4 pamene julliana adalowa form two . Atsikana onse adali anzeru kwambiri , madalitso adalemera kwambiri, adali otchuka koma ndi dzina loti hassan munzinda wa Blantyre , adafika pomayitanitsa ba bus akulu akulu aja anayi pakamodzi kuchokera maiko akunja . Madalitso adanenepa kwambiri , adagula nyumba yomanga manga munamiwawa . Kumpanda kwake kudali antchito ochuluka , . Agogo ake zinthu zimawayendera kwambiri , chaka chachinayi tapiwa adalemba mayeso omaliza amaneb, naye juliana adalemba jce .

Tapiwa amakana kupita kwawo holiday ikafika , pamene juliana amapita kwa agogo ake kumakawathandiza pa chigayo . Thupi la juliana amachita kuoneka ngati mwana wa bwana , samasowa kanthu.

Mayeso adatuluka juliana adakhonza bwino kwambiri , moti adabwelera kutauni kukapitiliza maphunziro ake .

Mayeso a form 4 adatuluka tapiwa adakhonza bwino kwambiri 10 points . Apa mkuti tapiwa akukwanitsa kuyendetsa galimoto moti amayendetsa yekha . Naye juliana adamuphunzitsa kuyendetsa galimoto atangofika form 3, kenako adamugulira yake .

Hassan hardware, hassan shopping centre, hassan tours transport, hassan wholesale. Paliponse dzina la hassan limapezeka munzinda wa Blantyre, . Nthawi zina julliana amazifunsa yekha kuti mchimwene mchifukwa chani adazisintha yekha dzina .

Moyo umapitilira , mwana, mkulu aliyense amalidziwa dzina la hassan ngakhale mwini wake asadamuone.

Chakachomaliza chidafika apa mkuti tapiwa ali ku CU kunguludi chaka choyamba , tapiwa mkuti akuyembekeza kulemba mayezo a 4 .

Hassan tsiku ndi mwezi wakufa adauzidwa ndi mfumu yakumadzi , mantha adayamba kumugwira hassan .......

Next part 12.....

Let's share to all groups.

Want your public figure to be the top-listed Public Figure in Ntaja?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Telephone

Address

Machinga
Ntaja