Edwin

Edwin

Share

Sports analysis
Manchester united fan

26/05/2026

NKHANI ZAMASEWERO ZA KU ULAYA.

πŸ“ Julian Alvarez khumbo lake akufuna atalowera ku timu ya Barcelona. Koma timu yake ya Atletico Madrid ikumugulitsa pa mtengo wosachepera €150m. Izi zipangitsa kuti timu ya Barcelona ilephere kumugula chifukwa mtengo ndi okwera kwambiri.

πŸ“ Sporting Director wa timu ya Barcelona, Deco, ali mdziko la England makamaka mu mzinda wa London kukapanga madongosolo ofuna kutenga katakwe omwetsa zigoli wa timu ya Chelsea, Joao Pedro.

πŸ“ Xabi Alonso akukomza zofuna kuphwasula squad ya Chelsea ncholinga chofuna kubweretsa ena atsopano. Ndipo waika pa msika osewera onse a Chelsea kupatulako osewera asanu okha omwe ndi; Pedro, Tosin, Cucurella, Palmer ndi Enzo.

πŸ“ Timu ya dziko la Ghana yatsimikiza kuti Muhammad Kudus sapezeka nawo mu squad yatimuyi yomwe ikupita ku World Cup mdziko la United States kamba kovulala.

πŸ“ Mphunzitsi wakale wa timu ya Chelsea, Enzo Maresca yemwe wangolembedwa kumene ntchito ku timu ya Manchester City, akukonza zokumana ndi kukambirana ndi Jack Grealish kuti abwerereso ku timu ya Manchester City.

πŸ“ Timu ya Atletico Madrid yakagogoda ku timu ya Barcelona ncholinga chofuna kugulako Marc Casado.

πŸ“ Pali chiyembekezo choti masabata akubwerawa chitsogolo cha milandu yokwana 115 yomwe timu ya Manchester City chidziwika. Matimu onse amu Premier League akuyembekezereka kudziwitsidwa za tsikuli.

πŸ“ Osewera a timu ya PSG, Ousmane Dembele komanso Hakim ayamba zokonzekera limodzi ndi anzawo lero pomwe akhala asakusewera kamba kovulala. Osewerawa akukonzekera kuthambitsana ndi timu ya Arsenal mu ndime yomaliza ya mpikisano wa UEFA Champions League.

πŸ“ Nico Paz akufuna kukhalabe ku timu ya Como season ikubwerayi. Tsopano Real Madrid ndiyomwe yatsala kupanga chiganizo chomutenga katswiriyu kapena ai.

πŸ“ Jose Mourinho wamudziwitsa kale president wa timu ya Real Madrid, Florentino Perez kuti akufuna kuonjezera osewera kutimuyi.

πŸ“ Ndi ma defender awiri okha atimu ya Real Madrid omwe ayitanidwa ndi matimu amayiko akwawo; Rudiger ndi David Alaba.

πŸ“ Matimu a Liverpool, PSG alowa nawo mchipiringu cholimbirana ndi timu ya Manchester United pa ntchito yofuna kutenga katakwe wa timu ya RB Leipzig, Yan Diomande. Ngati Diomande angalowere ku PSG, timu ya Liverpool idzafunitsitsa kutenga katakwe wa timu ya PSG Bradley Barcola.

Timu ya RB Leipzig ikumugulitsa Yan Diomande pa mtengo osachepera €100m.

πŸ“ Enzo Maresca watikitira mgwirizano wa zaka zitatu ku timu ya Manchester City.

πŸ“ Ngakhale zinavuta mu 2025, timu ya Tottenham Hotspur yabweranso kufuna kutenga osewera wa Manchester City, Savinho.

πŸ“Osewera wa timu ya Real Madrid, Toni Rudiger watikitira contract ina yokhalira kutimuyi mpaka 2027.
Osaiwala kupanga FOLLOW, SHARE, LIKE, COMMENT komanso INVITE anzanu kuti nkhanizi zisamakuphinyeni

23/05/2026

Manchester united yamupatsa contract carrick mwava bwanji ma red devils

20/05/2026
16/09/2025

These being your opponents pa ma elections awawa, they attack you from either flank, aaah watha basi πŸ˜‚πŸ˜‚

16/09/2025

Tickets are now available for sale. Visit your nearest access point and secure your seat for Sunday!

13/09/2025

Kodi game yamawa Manchester derby mkuyiwoona bwanji ma guy tichezepo lero

13/09/2025

Arsenal 3 0 forest
Zubemendi 2 goals
Viktor 1

10/09/2025

πŸ”πŸ”πŸ” ngakhale loan ya andrea onana ndi ya straight koma mwayi ozasewelaso ku man utd season ya mawa ndiwochepa

10/09/2025

Manchester derby ikhala yopanda omar marmoush kamba kovulala

10/09/2025

zayambika ku tnm super league πŸ’₯πŸ’₯πŸ’₯πŸ’₯πŸ’₯

Want your public figure to be the top-listed Public Figure in Mzuzu?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Website

Address

Mzuzu