Al Haqq Magazine

Al Haqq Magazine

Share

Registered at the GPO as a Newspaper
THE TRUTH - AUTHENTIC ISLAMIC INFORMATION FOR ALL

20/02/2026

Kusala kwachikakamizo monga kusala m’mwezi wa Ramadhan kumayenera kukhala ndi kutsimikiza za kusalako kuyambira kum’banda kucha kwa tsikulo.

18/02/2026

Ramadhan Karim our esteemed followers 🌙

18/02/2026

Kodi Khomo la Ar-Rayyan ndi chani?

Pangani like, comment komanso share uthengawu kuti ena apindule nawo.

17/02/2026

Babu Ar-Rayyaan 🫣🩶

16/02/2026

ARE YOU READY FOR THE BEST MONTH OF THE YEAR? 🌙

As we enter Ramadhan 1447, it is time to take stock of our faith and prepare our hearts for the blessings of Ramadhan. The latest issue of Al-Haqq Magazine (February 2026) is officially out!

In this issue, we explore:

Practical ways to prepare for the fast and increase our Iman.

Detailed Questions & Answers on the rulings of fasting, including travel and modern medical patches.

The Zakaat Nisaab update for this month: MWK 4,073,826.08.

find the download link in the comment section.

30/11/2025

Question

What rituals are to be done as per Sunnah and Islamic tradition for a new born baby?

Answer

There are certain rituals associated with child birth which are as follows: (1) After birth the Azaan should be recited in the child’s ear. (2) A tiny piece of date should be chewed well by the father or any pious person and then rubbed on the baby’s gum. (3) On the seventh day, the naming of the child should take place. On the same day his or her head should be shaved and the hair weighed. The equivalent of the hair in silver (l.e the cost of that weight of silver) should be given away in charity to the poor. (5) If the family can afford It, preferably on the same day, a goat or lamb should be distributed to the poor, family and friends in what is referred to as Aqeeqah. It is Sunnah to sacrifice two lambs if the child is a boy and one lamb if the child is a girl.

29/11/2025

Funso

Kodi mayi yemwe anakwatiwapo ndipo mwamuna wake anamwalira kapena kusiyidwa chabe, pofuna kukwatiwatinso ndikofunika kuti awuze makolo ake za zimenezi monga anachitira pachiyambi pamene amakwatiwa ali mtsikana kapena palibe vuto ngakhale makolo atapanda kuwuzidwa?

Yankho

Tinene zoti makolo ayenera kukhudzidwa pakukwatiwa kwa mwana wake pofuna kutsatira malamulo aChisilamu omwe amafuna kuteteza miyoyo ya anthu, kusunga ulemerero, chikhulupiliro, chuma komanso kuganiza kwa munthu. Choncho makolo amafunika pokwatiwa pa mwana wake pofuna kulemekeza mwambo ofunikirawu. Ngakhale kuti mkazi yemwe anakwatiwapo atha kukwatiwanso popanda makolo, ndibwino kuti makolo asasiyidwe padera pamene mkazi kapena mamuna akufuna kukwatira. Kwenikweni izi zili choncho pofuna kuonetsetsa kuti mkazi asakhale ngati wangotoledwa panjira powonetsatsanso kuti pali umboni wokwanira.

24/11/2025

Funso

Mnyamata wina akufuna kukwatira mtsikana yemwe kwanthawi yaitali wakhala akuchita zosalongosoka pochita zibwenzi ndi amuna osiyanasiyana. lye akuti akufuna kuchita izi pofuna kumuitanira mtsikanayo kunjira yabwino. Kodi kutero ndibwino?

Yankho

Ngati mtsikanayo akuonetsa kusintha kwa khalidwe lake lokonda amuna palibe chovuta kumukwatira. Koma ngati palibe kusinthika kwina kulikonse ndiye ndibwino kuganiza modekha musanamukwatire. Pakufunika kuti inu mukhale ndichitsimikizo chokwanira poti anthu ena amatha kungoyipitsa mbiri ya munthu wina.

23/11/2025

Funso
Ine ndasiyidwa banja kangapo konse. Kodi ndikoyenera kuti ndingokhala munthu wosakwatiwanso mpaka kalekale, chifukwa ndakonzeka kusachita zolakwika (zachiwerewere)?

Yankho

Ngati mukuona kuti sikoyenera kwainu kukhala pabanja ndipo mulibe chilakolako chokhala ndi mwamuna ndiye kuti palibe vuto inu kukhala osakwatiwa. Koma ngakhale izi zili choncho pofuna kulemekezeka ndikukhala moyo wauzimu wabwino ndibwino kukhala pabanja. Muyenera kukwatiwa chifukwa inu ndi munthu, pena mukhoza kufooka ndikukhala ndichilakolako chofuna mwamuna, poti ichi ndichilengedwe. Izi zingakupangiseni kuti musilire mwamuna yemwe sali wanu zimene zili zolakwika.

22/11/2025

Funso

Ine ndili ndi ngongole zambiri, moti sindikutha kukumbukira anthu ena omwe ndinawatengera ndalama zawo. Kodi pamenepa nditani?

Yankho

Yesetsani kuwapatsa iwo omwe mukuwakumbukira. Ngati anthu ena angabwere kudzaitanitsa ngongole ndipo ali ndi umboni wokwanira apatseni ndalama zawo. Komanso ngati mungakumbukire za munthu wina yemwe munatenga ndalama yake, koma simukudziwa komwe ali, muyenera kutenga ndalama imeneyo ndikupereka ngati Sadaqah m’malo mwaiye. Ngati atabwera pambuyo pake, muyenera kumufunsa ngati angavomereze za Sadaqah yomwe munapereka m’malo mwake. Ngati savomereza inu muyenera kumupatsa ndalama yake ndipo malipiro a Sadaqayo adzapita kwainu.

Al-Haqq November 2025 22/11/2025

Click to download Al-Haqq November 2025 edition

Al-Haqq November 2025 Click to download Al-Haqq November 2025

22/10/2025

Click the link to download Al-Haqq October 2025.
https://bit.ly/4qBLOxQ

Want your business to be the top-listed Media Company in Limbe?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Address

Globe Chambers
Limbe
BOX497,BLANTYRE