DSeven Smith
•Woyimba
•Mphunzitsi wazachilengedwe
Mawa tidzapange za Hippo, mukuona bwa🤔
15/10/2025
Kumawakonda makolowo kumeneko,chikondi chisaoneke lero lokha koma matsiku onse amoy wan✍
Happy Mothers Day to second mother👩👦🖤
10/10/2025
TAMVANI KANKHANI AKA👇😊
M’nyumba mwanga munali ziiiii m'mene ndimafika. Ili silinali bata lamtendere, koma bata lodabwitsa komanso kuchititsa mantha, tangoganizani olo phokoso olo🤔, bata kumachita kukhala ngati pansi pansuko. Ndinaima kwaka nthawi kuyang'anayang'ana ndipo nditazindikira kuti ngakhale kung’ung’udza kozoloŵereka kwa firiji kunali kusakumveka. Nditayang'ana chapatali ndi kumvetsera mwatcheru ndinazindikira kuti ngakhale wotchi yapakhoma sikumveka kaphokoso kake kaja.
Ine ndinazizimuka, tsitsi la m'mikono mwanga linayimirira ali mantha. kenako ndinati "Moni?"
Liwu langa silinamveke popeza silinamveke patali
Kenako Ndipamene ndinawona mwangozi,munthu wammuna. Anali atayima munjira yopita kuchipinda changa, ali chikhalire. Anali wamtali komanso wowonda, atavala suti yomwe imawoneka ngati imamwa kuwala, nsalu yakuda kwambiri yosapa mtundu komanso yosowa. Nkhope yake inali itagwetsedwa, kuyang'ana pansi pa kolidoyo.
Mpweya wanga unagunda.Chitseko changa chinali chokhomedwa pawiri.
Ndinayenda pang'onopang'ono, mwakachetechete kubwerera chakumbuyo ku kauntala yakukhitchini, kupita pamene pamakhala mipeni. Mmenemo ndekut mtima wanga ukugunda sizinaoneke. Ndinayang'ana m'njira.
Iye anali atapita.
Thukuta lozizira linatuluka pamphumi panga. Ndinayenera kuyimba thandizo. Foni yanga inali pa coffee table. Ndinatenga sitepe yonjenjemera kupita kuchipindacho, maso anga akuyang'ana uku ndi uku m'chipindacho. Munalibe chilichonse ndipo munali ziiiii.
Ndinatenga foni yanga ija. Koma network inali itathawiratu.
Ti!
Phokosolo linachokera kumbuyo kwanga,njira yochokera kukhitchini.
Ndinayang'ana kumbuyo. Bambo uja anali pomwepo, ali kumbuyo kwa ine, atayima kutsogolo kwa firiji. Iye anali kuyang'anitsitsa chithunzi chomwe ndidachimata ndi maginito pafirijipo - chithunzi cha ine ndi mlongo wanga pagombe la nyanja.
Iye anali pafupi kwambiri mwakuti ndimatha kuwona mmene ulusi wasuti yake yakuda unayendera, komanso momwe dzanja lake lotumbululuka, la zala zazitali lidatsata m'mphepete mwa chithunzicho.
Ndinasiya kupuma. Malingaliro anga anakuwa kwa ine kuti ndithawe, kuti ndifuule, kuti ndichite chinachake, koma thupi langa linali lozizira kwambiri. Uyu sanali wakuba. Ichi chinali china chake.
Pang'onopang'ono, anayamba kutembenuza mutu wake.. Kudali kozungulira pang'onopang'ono, mwadala, ngati dzanja la wotchi likusunthira ku ola lotsatira. Sindinafune kuwona nkhope yake.potengera ndi mmene manja ake amawonekera ndipo ndinaganiza kuti kuwona nkhope yake kukhala kutha kwa ine.
Ndinatseka maso anga.
Ndinayima pamenepo mwakachetechete wakuya, zikope zanga zidakulungidwa pamodzi.
Ndiye, ndinazimva kuti wafika kutsogolo kwanga.Ndinamva kununkhiza kwake tsopano—kununkhira kwa pepala lachikale losasunthika, fungo la wailesi yakanema yosiyidwa m’chipinda chopanda kanthu.
Mawu, owuma ngati fumbi ndi opanda phokoso ngati manda. Analankhula km izo sizinali m'makutu mwanga. Zinali m'mutu mwanga.
"Ukhoza kuyang'ana tsopano."
Maso anga anatseguka motsutsana ndi thupi langa....
Eeeeh anthu inu nthawiiii,timqlizabe😅😅
Ndimaliza mawa mamawa
08/10/2025
TAMVANI KANKHANI AKA👇😊
Nthaka yapadziko lonse inali youma ndi yong’aluka. Motero mkulu wina anati, "Palibe chomwe chingamerenso pano." Koma kamtsikana kena dzina lake Elara anapeza mbewu imodzi yosalira komanso yomaliza.Inali yaying'ono komanso yofiirira. Iye anayibzala m’fumbi. Tsiku lililonse ankathirira madontho angapo a madzi mbewu ija. Anthu anamuuza kuti akutaya nthawi potengera kuti madzi anali osowa zedi.Koma iye anapitiriza kuchita izo. Patapita milungu ingapo, katsamba kakang'ono kobiriwira kamene kanatulukira panthaka. Kanali kochepa kwambiri. Koma kanali kamoyo.
Mwaphunzira chani?😇
02/10/2025
IMVANI ZAMBIRI ZA RED LIPPED BATFISH
Nsomba yotchedwa red lipped batfish(Ogcocephalus darwin) ndi cholengedwa chomwe chimawoneka ngati ma cartoons potengera maonekedwe ake okhala ngati cartoon.Nazi zina mwazinthu zochititsa chidwi kwambiri za nsomba yapaderayi:
1. Ndi yosambira modabwitsa
-Nsomba ya red-lipped batfish ndi yodabwitsa kwambiri pakusambira. Zipsepse za pachifuwa, m'chiuno, ndi zakumbuyo zimasintha kagwiridwe ntchito kake ndikukhala ngati miyendo. -Imagwiritsa ntchito zipsepse zamphamvu izi pokuyenda pamtunda wamchenga kapena miyala yam'nyanja. Ikafuna kudutsa m’mbali mwa madzi, kusambira kwake nthawi zambiri kumakhala kovutirapo.
2. Milomo yake Siyopsopsonera
-Nsombayi imadziwika kwamviri fukwa cha milomo yake—milomo yake yowala komanso yofira ndi chinsinsi cha sayansi. Pali malingaliro angapo a ntchito za milomoyi:
a. kugwiritsidwa ntchito pokopa nsomba zina kuti zigonane , mofanana ndi mitundu yowala ya nyama zina zambiri.
b. CHimathandiza kuti nsomba za batfish zizizindikirana mumdima wozama.
-Mtundu wamulomo umabwera bwanji?---Asayansi ena amati mtunduwo umatha kubwera chifukwa cha zakudya za nsombayi.
3. Ili ndi nyambo kumutu kwake
-Ili ndi nyambo yaing'ono(yotchedwa esca) pamwamba pa mutu wake. Imagwedeza nyambo yamnofu imeneyi kuti ikope nyama zachidwi monga nsomba zazing'ono, nkhanu, ndi zina. Nyamayo ikayandikira kwambiri, nsomba yotchedwa batfish imapanga attack muma sekondi.
4. Ndi Nsomba imene imapezeka munyanja zikuluzikulu koma osati malo akuya kwambiri.
-Ngakhale kuti ili ndi maonekedwe odabwitsa ngati nyama ya m’nyanja yakuya, nsombayi simapezeka m’madzi akuya kwambiri. Imakhala kufupi ndi gombe la Zilumba za Galápagos ndi Peru, nthawi zambiri m'madzi ozama kuyambira 3 mpaka 76 metres. Anthu osambira,nthawi zina amakhala ndi mwayi wowona nsombazi
5. Imanunkhiza Chakudya Chake
"Nkhope" ya batfish kwenikweni ndi rostrum(beaklike), mawonekedwe a mafupa omwe amachititsa kuti ikhale ngati mphuno. Izi zimaganiziridwa kuti zimathandiza kuteteza nsomba ku nyama zolusa, komanso zimakhala ndi kachiwalo kakang'ono kamene kamagwiritsidwa ntchito yonunkhiza nyama zina m'madzi pamene zili pafupi ndikuwathandiza kupeza nyama mumdima.
6. Ndi atate odzibisa
-Matupi awo ndi otuwa, omwe amawathandiza kuti agwirizane bwino ndi mawonekedwe a mchenga wammadzi. Kubisala kumeneku ndikofunikira chifukwa kumathandiza kuti azigwira nyama zina zomwe zingoyendayenda
24/09/2025
Congratulations to His Excellency, Professor Arthur Peter Mutharika, on becoming the new President of Malawi.
This is a moment of great hope and promise for our nation. May your leadership be guided by wisdom, a deep commitment to the people of Malawi, and a vision for a peaceful and prosperous future.
We wish you strength and success as you lead Malawi forward.
Best wishes,
DSeven Smith
KODI MUKUDZIWA INU?
Akamapanga lipstick amaikamo mamba ansomba kuti azinyezimira
21/09/2025
TAMVANI KANKHANI AKA👇😊
Kamera yakalekale part2
Paja tinalekezera poti, Elara adajambula chithunzicho. Pachithunzichi, adadziwona yekha. Koma kumbuyo kwake kunali chinthu chachitali, chowonda. Chinalibe nkhope. Dzanja lake lalitali ndi la mafupa linali pa phewa lake.
Elara anachita mantha kwambiri. Anaponya kamera mu kabati yakukhitchini ndikuyitseka.
Elara sanagone. Anachita mantha kwambiri ndipo anadzidzidwa.
Patapita mlungu umodzi, iye anapita kuchipinda cha agogo ake chija. Anapeza bukhu lakale la agogo ake limene ankalembapo zinthu. Iye anawerenga izo.
Agogo ake aakazi anali atalemba kuti: "Kamera simawonetsa zakale ayi. Imawonetsa mizukwa. Nthawi zonse imakhala nafe chabe ndi yosawoneka. Koma Kamera imakulolani kuyiwona. Ndipo mukangoyiwona ... nayonso imayamba kukuwonani."
Chiganizo chomaliza chinati: "Umayima(mzukwa) pafupi ndi bedi langa usiku uliwonse. Ukudikirira kuti chithunzicho chimene ndinajambula chimalize."
Elara anachita mantha kwambiri mwakut anauma ndi mantha. Iye Amayenera kuwononga kamera. Anathamangira kukhitchini ndikutsegula kabati.
Kamera sanaipezemo, inali itapita.
Anamva phokoso kumbuyo kwake. Iye anatembenuka.
Kamera inali pa kauntala. Diso lake linali kuloza pa iye. Kenako, batani la shutter limayenda palokha.
Kuchokera m'chipinda chamdima, adamva phokoso. Phokoso la chithunzi chikujambulidwa. Chithunzicho chinali kumaliza.
Mpweya unazizira kwambiri. Khomo lachipinda chamdima linali lotseguka pang'ono. Kuwala kofiira kunawala kuchokera mkati.
Elara anachita mantha kwambiri kuti asunthe, koma amafunika kuona chithunzicho. Anayenda pang'onopang'ono kupita kuchitseko cha chipinda chamdima.
Chala chachitali, chotumbululuka, chinazungulira pakhomo ndikuyamba kumutsegulira chitseko kuti akawone chithunzi chake........ Mathero...
Mwina mukhoza kumazifunsa kuti "Kodi nkhaniyi yathera pamenepo, Eyah yatha.
Limenelo ndi funso labwino kwambiri. Nkhaniyi imatsirizidwa mwadala mwa njira yomwe imasiya mapeto odziwikiratu.
Pajatu Elara anapeza kamera, anapeza chinsinsi chake, ndipo tsopano wakhala chandamale, monga momwe analiri agogo ake. Nkhani ya themberero la kamera yatha.
·Apapa zoopsa zikukakwaniritsidwa popeza sizilinso pachithunzi koma mnyumba muja. Chimzukwa chija tsopano ndi chenicheni ndipo chili mnyumba mwake. Choyipa kwambiri chachitika.
Tawona tonse chimzukwa chija chikumuyitanira kuti aone chithunzi chomwe chajambulidwa.
Zinthu zimene zingathe kuchitika Elara akalowa m'chipinda ndi izi,
1. Akalowa, adzawona chithunzicho ndikugwidwa ndi mzukwa mpaka kalekale, monga agogo ake.
2. Chithunzichi chikhoza kusonyeza imfa yake.
3. Kuwona chithunzi chomaliza kungapangitse Chimzukwa chija kulowa mdziko lathu lapansi.
Mmenemo ndi m'mene ndikuganizira komanso m'mene nkhaniyi yathera. Ndikhulupirira mwamvetsetsa 😊
Mukhale ndi tsiku lopambana🙃
19/09/2025
TAMVANI KANKHANI AKA👇😊
Mutu: "Kamera yakalekale"
Agogo ake aakazi atamwalira, Elara ankakonzakonza m'nyumba yakale yagogowo. M’chipinda china chapamwamba, anapeza kamera yoti yakale yoti imangokhala.Inali yokongola komanso yolemera. Kamerayi inalembedwa mawu m'mbam'mbalimwake oti : "Solis Pictura" - kutanthauza "Chithunzi cha Dzuwa."
Elara ankakonda kujambula. Adapeza mpukutu wakale wa kanema ndikuwuyika mu kamera. Kamera inayamba kutentha. Anajambula chithunzi cha mpando umene agogo ake amawukonda.
Kamerayo inapanga kaphokoso. Utsi wawung'ono wasiliva unatuluka mu lens.
Pambuyo pake, chinatuluka chithunzicho. Chithunzicho sichinali champando wopanda kanthu icho chimaonetsa Agogo ake atakhala pampando ndipo Anali akumwetulira. Zinali zozizwitsa. Elara anasangalala kwambiri. Ankafuna kujambula zithunzi zambiri.
Gawo 2: The Shadow in the Photo
Tsiku lotsatira, Elara anatenga kamera kupita mumzinda(mtown) . Anajambula chithunzi cha mtsikana wina ku p**i. Atachikulitsa(atapanga zoom) , adawona kumbuyo kwa mtsikanayo kuli chithunzithunzi cha black ndipo chimaoneka choopsa.
Anatenga chithunzi china cha banja lina losangalala. Pachithunzichi, iwo ankawoneka akuchita mantha. Iwo anali kuyang'ana chinachake chowopsya kunja kwa chithunzicho.
Elara anachita mantha tsopano. Kamerayo simangojambula zithunzi za anthu, imajambula zithunzi za zinthu zoopsa zomwe zinali pafupi ndi iwo.
Usiku umenewo, anaganiza zojambula chithunzi chomaliza. Chithunzi chake. Anaitchera Kamerayo kuti ijambule kenako iyeyo anaima pakhoma.
Adajambula chithunzicho. Pachithunzichi, adadziwona yekha. Koma kumbuyo kwake kunali chinthu chachitali, chowonda. Chinalibe nkhope. Dzanja lake lalitali ndi la mafupa linali pa phewa lake.
Elara anachita mantha kwambiri. Anaponya kamera mu kabati yakukhitchini ndikuyitseka.
Mathero..........
Dikirani part 2 imene ili part yomaliza
Mukhale ndi tsiku lopambana 😊
Peter Mutharika-DPP (25,019)
Lazarus Chakwera-MCP (1,009)
Dalitso Kabambe-UTM (603)
NKHOTAKOTA
LIWALAZI CONSTITUENCY
Total final All Polling stations
APM - 10869
Chakwera - 4536
Ku constituency uku chigao chapakati ku chipinda kwa MCP koma wapambana ndi APM.
Anthu 9 sauzande analembesa kuzavota sanabwereko uku
Uthengau Ulandileni. Ndithu, ndithu
Click here to claim your Sponsored Listing.